spot_img
15.7 C
New York
Wednesday, May 15, 2024
spot_img

Aphungu a MCP avomereza ulimi wa Chamba

Aphungu a chipani cha Malawi Congress (MCP) avomereza lamulo lolola ulimi wa chamba m’dziko muno.

Aphungu wa avomera lamuloli mnyumba ya malamulo m’mawa la Lachinayi ponena kuti ulimi wa chamba utha kukweza chuma cha dziko lino.

Panthawi yomwe amavomeleza biluyi aphungu ena achipani cha DPP anatuluka mnyumbayi ponena kuti lamuloli ndilosayenera.

Malingana ndi aphungu wa, yemwe anabweresa bill yu a Peter Dimba sanafikire nthambi zingapo zokhudzidwa.

Koma, mtsogoleri wa zokambirana mnyumbayi a Richard Chimwendo Banda, wati cholinga cha biluyi sikuvomeleza kuti anthu adzisuta chamba koma kulima chambachi.

Ulimi wa chamba, malingana ndi a Dimba, utha kubweretsa ndalama zakunja mdziko muno zokwana pafupifupi 700 Million Dollars pa Chaka.

Related Articles

LEAVE A REPLY

Please enter your comment!
Please enter your name here

- Advertisement -

Latest Articles