spot_img
11.9 C
New York
Wednesday, May 1, 2024
spot_img

TIYENI TONSE TIKAPEREKE: Akhiristu a CCAP awalamula kupereka K10,000 aliyense  

Katswiri amene anapeka nyimbo ya ‘Ayambe Ku mbuyo ko, Ayambe ku mbuyo ko tikapereke eee, tiyeni tonse tikapereke’ m’kulinga anali ataziwona.

Lero mpingo wa CCAP mu Synod ya Blantyre yapempha akhiristu ake kupereka ndalama yokwana K10, 000 aliyense yothandizira kubweza ngongole yokwana K2 billion yomwe mpingo wu uli nayo.

Kalata yomwe yawelengedwa lero mipingo yonse yomwe yili pansi pa synod-yi, yalamulanso abusa onse kupereka ku Synod 10 kwacha pa 100 kwacha ili yonse ya chakhumi chomwe azitolera sabata ndi sabata.  

Malingana Mlembi wamkulu mu Synod ya Blantyre, Reverend Anderson Juma, zina mwa ngongolezi akuti ndi misonkho komanso zina zomwe Synod yi idatenga ku ma bank osiyasiyana m’dziko muno.

M’busa Juma anawonjezera kunena kuti ndalama zimene akhiristu a mpingo wu amapereka kudzera mu zopereka za malonjezano sizikukwanira poyendetsa ntchito za mpingo.

Ichi, ati n’chifukwa chake Synod ya Blantyre yakhala ikupempha akhiristu kuti azipereka molowa manja.

Related Articles

LEAVE A REPLY

Please enter your comment!
Please enter your name here

- Advertisement -

Latest Articles