Nduna Ya Achinyamata, a Richard Chimwendo Banda, alamula apolisi mādziko muno kuti afufuze bwino lomwe imfa ya Katswiri oyimba chamba cha Hip-Hop, Martin Nkhata amene amadziwika kuti Martse.
A Chimwendo Banda, omwe amayimilira mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera, ayakhula izi pa mwambo wa Maliro omwe wachitikira pa bwalo la Zamasewero la Civo, mu mzinda wa Lilongwe.
Nduna yo, yalamula a polisi wo, anthu omwe anali pa mwambo wa maliro wo, atakuwuza oyimilira aku banja, bambo Uchizi Nkhata, pa nthawi yomwe amafotokozera za imfa ya Martse, pomwe a Chimwendo ati kuti kufotokozera kwa akubanja kunali kosagwira mtima.
Māmawu awo a Nkhata, anati Martse anapita ku Mangochi ku kacheza, ndipo usiku wa Lachisanu, Iye {Martse} anachoka ku chipinda chomwe amagona kupita pa balaza kukaonjezera moto mu lamya yake ya māmanja.
Apa pomwe nyumba yo inayamba kuyaka moto, ndipo Malingana ndi a Nkhata, Martse pamodzi ndi anzake omwe anali mnyumba mo, anakwanitsa kuthawa, koma Martse anabwelera mnyumba moto uli mkati momwe anapsya kwambiri.
āPomwe moto unayamba kuyaka, iye pamodzi ndi anzake anakwanitsa kuthawa. Komatu, iye [Martse] anabwereranso mnyumba mo ndi kutseka chitseko,” anatero bambo Nkhata.
Martse wamwalira lolemba pa Chipatala Cha chikulu cha Queen Elizabeth chomwe mu mzinda wa Blantyre komwe amalandira nthandizo la mankhwala, kutsatira kupsya ndi moto ko.