Oweruza milandu ku bwalo lalikulu la milandu ku Lilongwe a Howard Pemba akana pempho la a Grezelder Jeffrey, amene amafuna kuti bwaloli lipereke chigamulo chamsanga choletsa mbali ya a Peter Mutharika kuchititsa msonkhano wa akuluakulu a chipani (NGC) mawa.
A Jeffrey, amene akutsutsa kuchotsedwa kwawo pa mpando wa mlembi wa chipanichi, amafuna bwaloli kuti lipereke chiletso choyembekezera choletsa a Clement Mwale, omwe asankhidwa kulowa mmalo mwawo, kuti asagwire ntchito iliyonse kuphatikizapo kuyitanitsa msonkhano wa mawawo.
Koma malinga ndi owayimira a Jeffrey pa mlanduwu a Cassius Chidothe, bwalo lati kuchita izi kutha kuchedwetsa chigamulo chachikulu pa mlanduwu.
Bwaloli lati lidzapereka chigamulo chake pa pempho la a Jeffrey pakatha masiku 5 kapena 7.
Woyimira mtsogoleri wa chipanichi, a Peter Mutharika, komanso chipanichi pa mlanduwu a Charles Mhango ati izi zikutanthauza kuti a Clement Mwale apitilira kugwira ntchito ngati mlembi wachipanichi mpaka chigamulo chitadzaperekedwa.
A Jeffrey adatengera a Mutharika, chipani cha DPP komanso a Mwale ku bwalo la milandu, kumene akufuna kuti bwaloli lichotse chiganizo cha a Mutharika chowachotsa pa mpando wa mlembi. (TIMES