spot_img
spot_img
8.8 C
New York
Friday, October 11, 2024
spot_img
spot_img

Timothy Mtambo wang’alura a Malawi

A Timothy Mtambo, omwe ndi m’modzi mwa anthu omenyera ufulu wa anthu m’dziko muno, wang’alura a Malawi omwe akhala akunene pa masamba a mchezo kuti iye “anatha” ndipo ndi “njoka yopanda mano m’kamwa”.

A Mtambo, omwe anakhalapo nduna m’boma la Dr. Lazarus Chakwera, ati iwo sanathe ndipo sanathepo.

Ndikudziwa kuti anthu makamaka pamasamba a mchezo akumati ndinatha. Ine sindinathe, ndipo sindinayambe ndatha,” a Mtambo, awuza a tolankhani lero ku Lilongwe.

Iwo amayankha pa funso lomwe anafunsidwa kuti athu ataya chikhulupiliro ndi iwo ngati omenyera ufulu.

A Mtambo ati iwo monga m’modzi mwa anthu omwe anavutika ndi utsi wokhetsa misonzi pa nthawi ya zionetsero zolimbana ndi DPP, apitilira kuyankhula pomwe zinthu sizikuyenda bwino.

M’mawu awo a Mtambo, anthu ambiri mdziko muno akukumana ndi mavuto kamba koti utsogoleri wa pano ukulephera kupanga ziganizo zoyenera.

Malingana ndi a Mtambo zomwe zikuchitika pano si zomwe anthu amayembekezera powonjezera kunena kuti chikumbumtima cha momwe anthu amavutikira ndi mvula komanso kuchitidwa nkhaza ndi apolisi pa nthawi ya zionesero chidakalipobe.

Related Articles

LEAVE A REPLY

Please enter your comment!
Please enter your name here

- Advertisement -

Latest Articles