spot_img
Saturday, December 14, 2024
spot_img
HomeLatestA Mutharika akulingalira zozapikisana nawo pa chisankho chamu 2025

A Mutharika akulingalira zozapikisana nawo pa chisankho chamu 2025

Mtsogoleri wa chipani cha Democratic Progressive (DPP) Professor Peter Mutharika wati akulingalira ngati azapikisane nawo pa chisankho cha mtsogoleri wa dziko lino m’chaka cha 2025.

A Mutharika anena izi pa msonkhano wa ndale omwe anachititsa Loweruka pa bwalo la masewero apa St Augustine 3 Primary School m’boma la Mangochi.

Iwo ati anthu ochuluka akuwafunsa kuti apikitsane nawo pa chisankho m’chaka cha 2025 ngati mtsogoleri wa dziko lino.

Apa a Mutharika ati akukhulupilira kuti chipani cha DPP chibweleranso m’boma posachedwapa kaamba koti Mgwirizano wa Tonse walephera.

Iwo ati chipani cha DPP mulibe kugawanika koma muli Mgwirizano ndipo anthu apitilire kusatila chipanichi.

Pa msonkhanowu panali anthu omwe aonetsa chidwi chopikitsana pa mpando wa mtsogoleri wa chipani cha DPP monga Dr. Kondwani Nankhumwa, Bright Msaka, Joseph Mwanamveka, George Chaponda mwa ena.

RELATED ARTICLES

LEAVE A REPLY

Please enter your comment!
Please enter your name here

- Advertisment -

Most Popular