spot_img
Thursday, December 12, 2024
spot_img
HomeLatestPDP ilowa m'boma chaka cha mawa, watero Kondwani Nankhumwa

PDP ilowa m’boma chaka cha mawa, watero Kondwani Nankhumwa

Mtsogoleri wa chipani cha PDP a Kondwani Nankhumwa ati akayamba ntchito amaimaliza ponena kuti chipani chawo chidzapambana pa chisankho cha chaka cha mawa.

Iwo amalankhula izi posachedwapa pomwe amatsekulira nsonkhano waukulu woyamba wa chipanichi ku Comesa hall mu mzinda wa Blantyre.

A Nankhumwa ati sakanayambitsa chipani cha PDP akudziwa kuti adzalephera potsindika kuti adzalowa m’boma chaka cha mawa.

Mwa maudindo makumi atatu (30) omwe anthu akuyembekezeka kupikisana pachisankho cha atsogoleri atsopano achi maudindo 22 anthu adutsa opanda opikisana naye.

Ena mwa omwe adutse opanda opikisana nawo ndi mtsogoleri wogwilizira wachipanichi a Nankhumwa, wogwilizira udindo wamneneri wachipanichi a Rhodes Msonkho ndi a Austin Nsopela, paudindo wa mkulu wa achinyamata.

RELATED ARTICLES

LEAVE A REPLY

Please enter your comment!
Please enter your name here

- Advertisment -

Most Popular