spot_img
Sunday, December 15, 2024
spot_img
HomeLatestMusaope ngongole, mukaopa muzagona ndi njara- MCP yauza a Malawi omwe akukutika...

Musaope ngongole, mukaopa muzagona ndi njara- MCP yauza a Malawi omwe akukutika ndi umphawi

Wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipani cha Malawi Congress (MCP) a Catherine Gotani-Hara ati anthu asamaope kutenga ngongole ya NEEF.

A Hara ayankhula izi pa bwalo la St. Martin’s ku Zomba Thondwe lero Lamulungu pa msonkhano wa ndale.

Malingana ndi a Gotani Hara, omwenso ndi sipikala wa nyumba ya malamulo, ngongole ya NEEF ndi ya Amalawi eniake, chomcho asawope kukatenga.

Pamenepa, mayi Gotani Hara ati aonetsetsa kuti adindo atengepo gawo pothandiza Amalawi kutenga ngongolezi.

Pa nkhani ya njara yomwe yafipa povuta m’dziko muno, a Gotani-Hara, atsimimikizira anthu aku Zomba kuti alandira chimanga.

M’mawu awo, a Gotani-Hara atinso mtsogoleri wa dziko lino, a Lazarus Chakwera, akufuna dziko lino likhale ndi chakudya chochuluka.

Iwo ati, ichi ndi chifukwa chake boma la a Chakwera laakhazikitsa ntchito za ma Mega Farms pofuna kukwaniritsa izi.

RELATED ARTICLES

LEAVE A REPLY

Please enter your comment!
Please enter your name here

- Advertisment -

Most Popular