spot_img
Thursday, December 12, 2024
spot_img
HomeLatestMatako akhalabe m'manja mwa apolisi

Matako akhalabe m’manja mwa apolisi

Oweruza wa ku bwalo la Senior resident Magistrate m’boma la Balaka, Joshua Nkhono lero wakana kupeleka belo kwa mayi Lilian Matako ndi amuna ena awiri omwe akuwaganizira kuti anachita zinthu zofuna kuvulaza munthu.

Anthuwa omwe ndi kuphatikizapo a Zuberi Chitete komanso a Ishmael Chitete adanjatidwa zitadziwika kuti adathandizana kupereka chilango chomangilira ku mtengo komanso kuthira madzi a chitedze kwa mwana wa zaka 9 pomuganizira kuti anaba ndalama yokwana K2,000.

Powonekera ku bwalo la milandu lero masana, anthuwa akana kuvomera mulandu omwe mbali ya boma yatsegulira m’bwalo la milanduli.

Malipoti akuti a Matako, omwe ndi a zaka 28 ndipo ndi mayi ake a mwanayu, amachita bizinesi ndipo tsiku lina akuti anasiya ndalamayo kuchipinda kwawo yomwe pobwelera, sanayipeze.

Apolisi anati izi zidapangitsa kuti amupanikize ndi mafunso mwanayo kufikira pomwe anaulura kuti anabadi ndalamayo zome zinachititsa kuti amupase chilango chotero mothandizana ndi anthu a Zuberi komanso a Ishmael Chitete.

Kumva mlanduwu kupitilira lachisanu sabata ino pomwe bwalo lidzawunikile pa pempho lawo la belo.

Oganizilidwawa amachokera m’mudzi mwa Kanyumbaka, mfumu yaikulu Sawali m’boma lomweri la Balaka.

RELATED ARTICLES

LEAVE A REPLY

Please enter your comment!
Please enter your name here

- Advertisment -

Most Popular