spot_img
Saturday, December 14, 2024
spot_img
HomeLatestZaka 12 ku ndende kamba kokakamiza mwana kumuyamwa 'mabatire'

Zaka 12 ku ndende kamba kokakamiza mwana kumuyamwa ‘mabatire’

Bwalo lamilandu ku Balaka lalamula bambo wazaka 38 Kefasi Kambanizithe kakakhala ku ndende kwa zaka khumi ndi ziwiri (12) kamba kokamiza nyamata wa zaka zisanu kuti amuseweretse ndi kuyamwa maliseche.

Oyimilira boma pa mlandu Liston Sabola anauza bwalo kuti mkuluyu anaimitsa nyamatayu ndikumuvula ndipo anamuyamwa maliseche uku ukumuopyeza kuti asakuwe.

Kenaka mkuluyu anamukakamiza mwanayu kuti nayenso amuyamwe maliseche ake.

Atatero mkuluyu anamupatsa mwanayu MK100 kuti asaulule.

Koma mwanayu anawauza amayi ake omwe anadziwitsa apolisi ndipo kutsatira kafukufuku mkuluyu anamangidwa.

Ndipo pokumva mulanduwu, oganiziridwayu anayamba ndi kukana ndipo apolisi anabweretsa mboni zinayi.

Ndipo atapezeka olakwa mkuluyu anapempha kuti akhulikilidwe kamba koti ndi munthu oti amathandiza banja lake komanso ali ndi ulemu.

Koma oweruza milandu Joshua Nkhono anati mchitidwewu siwabwino ndipo wapereka chilango cha zaka khumi ndi ziwiri (12).

Kambanizithe amachokera mmudzi wa Chilobwe, dera la kwa Kachenga ku Balaka.

RELATED ARTICLES

LEAVE A REPLY

Please enter your comment!
Please enter your name here

- Advertisment -

Most Popular