spot_img
21.5 C
New York
Monday, June 17, 2024
spot_img

Nsazurwimo Ramadhan “watamanga”

Mphunzitsi wamkulu wa timu ya Mighty Mukuru Wanderers, Nsazurwimo Ramadhan, wati watula pansi udindowu kutsatira kugonja kwa timuyi mumasewero awiri motsatizana mu TNM Super League.

Ramadhan, yemwe adalonjeza kubweretsa chimwemwe kubanja la Manoma, waona ngati kumaloto atagonja ndi timu ya Mzuzu City Hammers ndi zigoli ziwiri kwa duu loweruka patangopita masiku ochepa timuyi itagonjaso ndi timu ya Silver Strikers ndi zigolinso ziwiri kwa duu.

Ramadhan, popereka kalata yotula pansi kwa mtsogoleri wa timuyi Thom Mpinganjira, wati sakufuna kukakamiza zinthu.

“Ngati tebulo silikufuna kukupatsa chakudya kulibwino kuzisiya,” iye watero.

Timu ya Wanderers ili ndi mapointi khumi ndi awiri pamndandanda wa matimu omwe akusewera mu ligi yaikuluyi ndipo ikusiyana ndi mapointi khumi ndi timu yomwe ikutsogola ya Silver Strikers ndipo onse asewera masewero okwana asanu ndi atatu.

Related Articles

LEAVE A REPLY

Please enter your comment!
Please enter your name here

- Advertisement -

Latest Articles