spot_img
Friday, December 13, 2024
spot_img
HomeLatestNyengo ya Ramadan ndiyofunikira kwambiri Kwa Asilamu – Mutharika

Nyengo ya Ramadan ndiyofunikira kwambiri Kwa Asilamu – Mutharika

Mtsogoleri wa chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) a Professor Peter Mutharika, lero anakachezera asilamu pa mzikiti wa ukulu (Main Mosque) omwe uli mu town ya Mangochi.

A Mutharika, omwenso ndi mtsogoleri wakale wa dziko lino, anapita kukachezera asilamuwa pamene ali m’nyengo yosala kudya ya Ramadan.

M’mawu awo a Mutharika, ati nyengo ya Ramadan ndiyofunikira kwambiri chifukwa nthawiyi imawayandikitsa asilamuwa ndi Allah posala kudya komanso kuchita ntchito za chifundo (Zakaat).

A Mutharika anatinso apitiliza kucheza m’mizikiti yosiyanasiyana m’dziko muno chifukwa amazindikila kufunika kwa Ramadan.

Ndipo polankhulapo, Mfumu ya delari a Mgundaphiri anathokoza a Mutharika pochezera anthu achipembedzochi.

Mtsogoleri wakaleyu anapereka zakudya monga mpunga, sugar komanso ufa zoti anthu azimasulira Ramadan.

Iwo adaperekezedwa ndi Mai akunyumba kwawo a Getrude Mutharika komanso a Sameer Suleman MP, a Ralph Jooma, Sheik Salire Saidi komanso akuluakulu a mpingo wa chisilamu m’bomalo.

RELATED ARTICLES

LEAVE A REPLY

Please enter your comment!
Please enter your name here

- Advertisment -

Most Popular