spot_img
21.7 C
New York
Sunday, September 26, 2021

Buy now

spot_img

Evance Meleka’s Nthata Za Njala Goes Viral

Malawi Music

Artist: Evance Meleka

Song title: Nthata za njala

Music genre: local Raggae

Intro

Oh ooh! oh oh oh oh oh! uyo! (x 2) mayo!

Verse 1

Chinali chigalu chobeba gogo ali ndi moyo, chinkasamalidwa chinalibe nthata, atangomwalira mwini wake wa galu! lero galu nthiti zawonekela.

Zaka zapitazo linali ngati phwando, nthata zinasowetsa Mtendere galu, mkulu wina wozala ndi Chifundo! anamupempha galu ndikusatse nthata.

Koma galu analira mokana! musandichotse nthata zokhutakhuta! Mukachotsa izi pabwera nthata zanjala, zizangomaliza kamoyo Kangaka.

Mkulu wa Chifundo nikakamila! Kuthothola nthata pathupi la galu, lero ndi izi pagwa nthata zanjala! tikunena pano, galu chikomokele.

Chorus

Lead: Nthata za njala!
Backing vocals: Nthata za njala!

Lead: Nthata za njala!
Backing vocals: Nthata za njala!

Lead: oh oh oh oh!
Baking vocals: Nthata za njala!

Lead: Eeeeee!
Backing vocals: ndizomwe zitamalize umoyo wa galu!

Lead: Zangochoka kudzuwa!
Backing vocals: Nthata za njala!

Lead: Nthata za njala!
Backing vocals: Nthata za njala!

Lead: Ndikunena nthata za njala
Backing vocals: Nthata za njala!

Lead: Eeeeee!
Backing Vocals: ndizomwe zitamalize umoyo wa galu.

Verse 2

Vuto ndaliwonana sinkulu wachifundo! cholinga Chinali galu apeze mpumulo, Koma kuti nthata zangopezela mwayi, kuyikama ng’ombe yoti ndiyowonda kale.

Nthata zokhazokha zayamba kulimbana! ati galuyu ndinamupeza ndine, zokhazokha zikungokokanakokana, chimvano ichi sin’kuchiwona bwino.

Nanjinanji kwatigwera chigodola! sindidziwa ngati galu atapulumuke, poti ndalama zothetsera chiwewe! anthu adyela anazichita phwando.

Akulu achifundo bwanji musatope, ntchito yabwino munayiyamba kale! mukalekelela nthata izizi, ziwononga mbiri yanu yabwino ija.

Chorus

Lead: Nthata za njala!
Backing vocals: Nthata za njala!

Lead: Nthata za njala!
Backing vocals: Nthata za njala!

Lead: oh oh oh oh!
Baking vocals: Nthata za njala!

Lead: Eeeeee!
Backing vocals: ndizomwe zitamalize umoyo wa galu!

Lead: Zangochoka kudzuwa!
Backing vocals: Nthatag za njala!

Lead: Nthata za njala!
Backing vocals: Nthata za njala!

Lead: Ndikunena nthata za njala
Backing vocals: Nthata za njala!

Lead: Eeeeee!
Backing Vocals: ndizomwe zitamalize umoyo wa galu.

Verse 3

Mtsogolomu nyombiyi ipitilira! Koma kwalero bwanji ithere pompa?Ndangodutsa sindinathyole nkhwani,ndakusokosani n’kulinga mutamba.

Muvi wolekelera! umalasa m’maso, gwirani ntchito kukalima mawa, opaleshoni kukachotsa nthata.

Chorus

Lead: Nthata za njala!
Backing vocals: Nthata za njala!

Lead: Nthata za njala!
Backing vocals: Nthata za njala!

Lead: oh oh oh oh!
Baking vocals: Nthata za njala!

Lead: Eeeeee!
Backing vocals: ndizomwe zitamalize umoyo wa galu!

Lead: Zangochoka kudzuwa!
Backing vocals: Nthata za njala!

Lead: Nthata za njala!
Backing vocals: Nthata za njala!

Lead: Ndikunena nthata za njala
Backing vocals: Nthata za njala!

Lead: Eeeeee!
Backing Vocals: ndizomwe zitamalize umoyo wa galu.

Related Articles

1 COMMENT

LEAVE A REPLY

Please enter your comment!
Please enter your name here

- Advertisement -

Latest Articles