spot_img
Saturday, December 14, 2024
spot_img
HomeLatestNankhumwa pachiwongolero cha PDP

Nankhumwa pachiwongolero cha PDP

Nthumwi zomwe zili kumsonkhano osankha adindo achipani cha PDP zatsimikiza kuti a Kondwani Nankhumwa ndiwo mtsogoleri wachipanichi kwa zaka zisanu zikubwerazi ndipo iwo adutsa popanda opikisana naye.

Msonkhano osankha adindo wu ukuchitikira ku Comesa Hall mumzinda wa Blantyre, ndipo wayamba dzulo.

Nthumwizi zasankhanso a Rose Sagala kukhala wachiwiri kwa mtsogoleri wachipanichi pomwe a Semion Phiri ndiwo awasankha kukhala mlembi wamkulu wachipanichi.

A Nanariwa Nanguwo awasankha kukhala mkulu woona zachisankho mchipanichi, a Kondwani Kumitengo ndimkulu woona zamalamulo, a Rhodes Msonkho ndi mneneri wachipanichi ndipo a Kettie Mkandawire ndi mkulu woona zokonza zochitika mchipanichi.

RELATED ARTICLES

LEAVE A REPLY

Please enter your comment!
Please enter your name here

- Advertisment -

Most Popular