spot_img
Saturday, December 14, 2024
spot_img
HomeLatestChakwela amukwidzinga nawo unyolo

Chakwela amukwidzinga nawo unyolo

A polisi ya Deayang pansi pa polisi ya Kanengo amanga anthu awiri powaganizira mlandu wakuba.

Mneneli wa polisi ya Kanengo Gresham Ngwira wati omangidwawa ndi Notice Chakwela wa zaka 31 komanso Yohane Mauzeni wa zaka 33.

Iwo ati awiriwa akhala akukhudzidwa ndi umbava omwe wakhala ukuchitika madera osiyanasiyana kuyambira mu December chaka chatha kufikira mwezi uno.

Atachita kafukufuku a polisi adakwanitsa kupeza Chakwela ku Nchezi ndipo pa nthawi yomwe amamumanga mkuluyu adayamba kulimbana ndi a polisi kufikira pomwe apolisi adamuombera pamwendo.

Makosana awiriwa omwe amakhala kwa Mgona ku Lilongwe, apezeka ndi katundu osiyanasiyana monga ma solar panels, ma lamya awiri komanso ma battery a galimoto akulu akulu.

A Ngwira ati awiriwa, omwe adagwirako jele pa milandu ngati yomweyi, akaonekera ku bwalo la milandu posachedwapa komwe akayankhe mlanduwu.-( By Promise Thom, Nkhoma Synod Radio)

RELATED ARTICLES

LEAVE A REPLY

Please enter your comment!
Please enter your name here

- Advertisment -

Most Popular