spot_img
19.7 C
New York
Saturday, June 15, 2024
spot_img

Sitikufuna Cyclone pakati pa a Chakwera ndi a Chilima – Usi

Nduna ya za chilengedwe, a Michael Usi,ati iwo sakufuna namondwe wa ndale amene anthu amakolezera pakati pa mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera ndi achiwiri awo, Dr Saulos Chilima.

Iwo anena izi lero La Chitatu m’boma la Mulanje pa mwambo woyatsa mekendulo pokumbukira anthu omwe anamwalira kaamba ka Namondwe wa Freddy m’maboma ena m’chigawo chaku mwera.  

M’mawu awo a Usi ati pali anthu ena omwe amakonda kuyankhula zambiri zokhuza a Chakwera ndi a Chilima ndicholinga chofuna kudzetsa mpungwepungwe.

“Sitikufuna Cyclone pakati pa awiriwa,” watero Usi, yemwe ndi m’modzi mwa akulu akulu a chipani cha UTM.

M’buyomu mtsogoleri wa dziko lino a Chakwera anauza a Malawi kuti pali kagulu kena ka anthu komwe kakufuna ku wayambanitsa iwo ndi wachiwiri wawo a Chilima.   

Malingana ndi a Chakwera, anthu ena amakonda kudanitsa komanso kuyambanitsa anthu ndipo ayesera kangapo konse kudanitsa iwo ndi a Chilima koma alephera.

“Ndikuziwa kuti pali anthu ena omwe akufuna kutiyambinitsa ndi a Chilima komanso zina mwa nduna zanga,” anatero a Chakwera

Malingana ndi a Chakwera, iwo sapanga nawo ndale zodanitsa, zotukwana ena komanso zonyoza ena.

Pamenepo a Chakwera anapempha a Malawi komanso a ndale ena kuti asiye ndale zosungirana ka m’peni ku mphasa.  

Pakhala pali phekesera zoti a Chakwera omwe ndi a chipani cha Malawi Congress (MCP) komanso a chiwiri awo a Chilima a chipani cha UTM akhala asakugwirizana.

Related Articles

LEAVE A REPLY

Please enter your comment!
Please enter your name here

- Advertisement -

Latest Articles