spot_img
Sunday, December 15, 2024
spot_img
HomeLatestMalamulo akumulola Chilima kuyima-UTM

Malamulo akumulola Chilima kuyima-UTM

Chipani cha UTM chatsutsa malipoti akuti wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino yemweso ndi mtsogoleri wa chipanichi,Saulos Chilima sali woyenera kudzapikisana nawo pa mpando wa utsogoleri wa dziko pa chisankho cha chaka cha m’mawa.

Izi zikudza pomwe anthu ambiri pa masamba a m’chezo akhala akuyankhula kuti Chilima sali woyenera kudzaimira nawo pa mpando wa utsogoleri wa dziko lino malingana ndi malamulo.

Koma m’neneri wa chipanichi, Felix Njawala wawuza Timveni Online kuti malamulo akumulola Chilima ngakhale wakhala wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino kwa materemu awiri.

Njawala wati pali anthu ena omwe akufalitsa nkhanizi mwadala ndi cholinga chongofuna kusokoneza komanso kuchotsa chidwi cha a Malawi pa a Chilima. – (Credit Alex Batison, Timveni Online).

RELATED ARTICLES

LEAVE A REPLY

Please enter your comment!
Please enter your name here

- Advertisment -

Most Popular