spot_img
18.9 C
New York
Sunday, May 26, 2024
spot_img

Mayere agwera a Dr. George Chaponda

Chipani chachikulu chotsutsa boma cha Democratic Progressive (DPP) chasitika dzina la a Dr. George Chaponda pa udindo wa mtsogoleri wa zipani zotsutsa boma ku nyumba ya malamulo.

Chaponda, yemwe ndi phungu wa nyumba ya malamulo wa m’dera Mulanje South, alowa m’malo mwa a Kondwani Nankhumwa omwe achotsedwa mu chipani DPP kaamba kosowekera mwambo.

Mlembi wamkulu wa chipanichi a Clement Mwale, ati a Dr. Chaponda ali ndi kuthekera kogwira ntchitoyi mokhulupilika kaamba koti ndi m’modzi mwa am’khalakale pa ndale m’dziko muno.

Chipani cha DPP chakhala chisakukondwa ndi a Nankhumwa, amene ndi phungu wa m’dera la Mulanje Central, kukhala pa udindowu.

Kangapo konse Mneneri wa chipanichi a Shadric Namalomba akhala akunena kuti a Nankhumwa anasankhidwa pa udindowu ndi chipani cha Malawi Congress (MCP).

Related Articles

LEAVE A REPLY

Please enter your comment!
Please enter your name here

- Advertisement -

Latest Articles