spot_imgspot_img
Saturday, March 22, 2025
spot_img
spot_img
HomeEntertainmentAmuyamukira Pochotsa Amapiano ku Gospel

Amuyamukira Pochotsa Amapiano ku Gospel

Anthu otsatira nyimbo zaumzimu, makamaka omutsatira Stevie Wazisomo Muliya, ayamikira katswiriyu pa nyimbo yomwe watulutsa lero ya “Mwatikhalira wabwino”.

Muzaka ziwili zapitazi anthu akhala akuzuzula katswiri yu, ponena kuti Amapiano chi chamba cha gospel.

Malingana ndi zomwe anthu alemba mmatsamba a ambiri Nchezo( Facebook), pomwe nyimboyi waonetsedwa koyamba, anthu ochuluka awonetsa kukhutira kuti Wazisomo watsata njira yabwino ya maimbidwe kusiyana ndi momwe amachitira mmbuyomu poyimba chamba cha Amapiano.

“Muliya koma uyuyu, osati wa Amapiano uja”, watero otsatira wina yemwe dzina lake ndi Mike AlibeWawo.

“Eya ife timafuna zimenezi, osati Amapiano”, watero wina, Kondwani Stephano Batson.

“Mwatikhalira Wabwino” ndi nyimbo yomwe Stevie Wazisomo( Mr Grace) watulitsa ndipo ili mu chamba Cha Praise and Worship, yomwe yajambulidwa ndi OBK ndipo video yake yajambulidwa ndi VJ ken

RELATED ARTICLES

1 COMMENT

LEAVE A REPLY

Please enter your comment!
Please enter your name here

- Advertisment -

Most Popular