spot_img
Friday, December 13, 2024
spot_img
HomeLatestNKHONDO YA MKACHITSI: Mpingo wa Bangwe SDA wagawana zida.

NKHONDO YA MKACHITSI: Mpingo wa Bangwe SDA wagawana zida.

….Atsogoleri athu akukhala ngati “Asatana”

Philadelfia, chikondi cha abale chathapo, mpesa uja ukupitilira kuwawa pomwe ka gulu kena pa mpingo wa Bangwe Seventh Day Adventist kawukila mpingo wu.

Malingana ndi kalata yomwe tawona, ka gulu ka kati sikakukondwa ndi momwe akuluakulu ena apa mpingowu akuyendetsera zinthu, ponena kuti sizikusiyana ndi zomwe Satana anachita ku mwamba, inde kufuna kuwoneka wa mkulu kuposa Mulungu.

“Ife tikudabwa kuti akulu akulu athu akukana kukumana ndi kholo lanthu kuti amvane chimodzi,” anatero m’modzi mwa anthu ogalukirawa.

Izi zachitika patangopita masiku ochepa akulu akulu a mpingo wa SDA pansi pa South Malawi Conference atalengeza kuti achotsa mpingo wa Bangwe SDA mu kaundula kaamba kokula “mtima komanso kudelera mfundo za mpingo”.

Malingana ndi uthenga omwe ukuwulutsidwa pa wayilesi ya SDA, ganizo lochotsa Bangwe SDA mu mpingowu m’dziko muno likakambidwa mu December chaka chino pa mkumano wa akuluakulu a SMC, ndipo akhrisitu omwe akufuna kupitilira kukhalabe ma membala a SDA, awuzidwa kuti atuluke Bangwe SDA.

“Izi zikutanthawuza kuti mpingo wa Bangwe SDA udzaleka kukhala wa SDA ngati ganizoli likavomelezedwe ndi nthumwi za session.

Pa chifukwa ichi atsogoleri a SMC akulangiza akhilisitu aku Bangwe SDA omwe akufunabe kukhala akhilisitu a SDA kuti akalembetse mayina awo ku ofesi ya SMC, ku Sunnyside, Blantyre mu ofesi ya mlembi wamkuku wa SMC pasanafike pa 25 November 2024, ndipo akuchenjeza kuti akapanda kutelo azaleka kukhala akhilisitu a mpingo wa SDA,” yatelo mbali ina ya uthengawo.

SMC yadandaula kuti pa 15 June, 2024, atsogoleri ake ena omwe adapita ku Bangwe SDA kuti akapeleke uthengawu, sadapatsidwe mpata oyankhula pomwe akhilisitu kumeneko patsikuli ankangoyimba nyimbo mokweza ndi mosalekeza mpaka mamulumuzanawo atatopa adanyamuka kubwelera.

Mwazina Bangwe SDA ikudzudzulidwa kuti siimalola amayi kulalikira, ikugwiritsa ntchito chizindikiro cha angelo atatu chomwe chimkagwilitsidwa ntchito kalekale komanso kuphunzitsa ziphunzitso zina zotsutsana ndi malamulo a mpingo wa SDA.

Akhilisitu ena ku Bangwe SDA atitsina khutu kuti iwo samafuna kugwiritsa ntchito chizindikiro chatsopano cha mpingowu (logo) chomwe chili ndi lawi, mtanda komaso baibulo, ponena kuti anthu otsatira “chirombo” ndi omwe amayika mtanda pa guwa ndikumaurambira.

Chizindikiro chakale chomwe Bangwe SDA ikugwiritsabe ntchito chili ndi angelo atatu aliyese atanyamula lipenga.

RELATED ARTICLES

LEAVE A REPLY

Please enter your comment!
Please enter your name here

- Advertisment -

Most Popular