spot_img
Friday, December 13, 2024
spot_img
HomeLatestSamuel wayankha kawiri pokupha Baka

Samuel wayankha kawiri pokupha Baka

Timu ya Kamuzu Barracks yakwanitsa koyamba kugoletsa kanayi mu ligi ya TNM pamene agagada Baka City 4-0 pa bwalo lamasewero la Aubrey Dimba kwa Kapiri m’boma la Mchinji.

Uku kunali kupambana koyamba m’chigawo chachiwiri mu ligiyi ndipo zikukutanthauza kuti pa mndandanda wamatimu, asilikaliwa ali pa chisanu ndi ma point 28 pa masewero 18, pomwe Baka City ndiyotsiriza ndi ma point 8 okha.

Patangodutsa mphindi zisanu ndi zinayi pamasewerowa, osewera otchinga kumbuyo a Baka adagwetsa katakwe amene ali pa chiongolero cha ochinya mu ligiyi, Zeliat Nkhoma, zomwe zinapangitsa kuti oyimbira masewerowa, Luckson Chunda, ayimbe pinto ndi kupereka Free Kick yomwe adamwetsa ndi Samuel Gunda.

Koma zinaoneka kuti golo limene panakhala Abraham Mwandenga wa Baka City linayitananso a Gunda patangotha mphindi khumi zokha chigoletsereni kuti aponyerenso mpira mu ukonde.

Mphindi zisanu ndi ziwiri zitadutsa, Zeliat anakhoma nsomali wa chigoli chachitatu atalandira mpira wosemedwa bwino ndi Martias Nyirenda.

Koma phwando la Kamuzu Barracks silinathere pomwepa, chifukwa Gregory Nachipo anabaya chigoli chachinayi pa mphindi yachi 90.

Kuyankha komaliza kwa Samuel kunali kumene anakamupatsa mendulo ya osewera bwino m’masewerawa.

Komabe, mphunzitsi wa KB, a Charles Kamanga, anati masewerowa anali ovuta kwambiri.

“M’mene tinakonzekera ndi zimene takwaniritsa. Tinawina kalekale pa 30 May [2-1 atapilipintha Karonga United],” anatero a Kamanga.

Ndipo mbali yawo A Davie Kayamira, amene ndi wachiwiri kwa mphunzitsi wa Baka City, anati sanayambe bwino masewerowa chifukwa samayembekeza kuti adani awo abwera mwaukali.

“Anyamata anakayamba masewerowa ngati m’mene tinachitira m’chigawo cha chiwiri, tikanapambana. Komabe kungoti tatenga ana aku reserve,” a Kayimira anatero.

Masana omwewa, m’boma la Dedza, Gift Magola anapatsa mphatso timu yake ya Premier Bet Dedza Dynamos pochinya chigoli chokhacho pa mphindi 71 kuti agonjetse FOMO FC.

Apa ndiyekuti Dedza Dynamos ili pa nambala yachi khumi ndi ma point 23 pamasewero 18, pomwe FOMO ili pa nambala 14 ndi ma point 15 pamasewero 18.

Mphunzitsi wa Dedza, a Andrew Bunya, anati a FOMO anapita m’bomalo ndi cholinga chifukwa samawapatsa mpata komabe atasintha zinthu zingapo ndi zimene zinawapangitsa kuti apambane.

FOMO anayiyankhulira ndi mphunzitsi wa agoloboyi awo, Charles Chikoti, ndipo anati sakuyang’ana pansi ngakhale agonja pofuna kuyamba kupambana.

Nkhondo yofuna kupeza katswiri wa ligiyi ibweranso loweruka sabata ya mawa, ndipo amene akusungira chikho cha ligiyi, FCB Nyasa Big Bullets adzafikira kuonetsana chamuna ndi Dedza pa bwalo masewero la Kamuzu mu mzinda wa Blantyre. Pomwe ku Chiwembe, Bangwe idzakumana ndi FOMO.

Tsiku lomwelo, m’boma la Nkhotakota kudzakhala nkhondo yapachiweniweni ya asilikali pamene MAFCO idzaonane maso ndi maso ndi Moyale Barracks.

Sabata yomweyo, amene ali pa chiongolero mu ligiyi, Silver Strikers, adzakhala ku chigawo cha ku mpoto kuti akatibulane ndi timu ya Chitipa United.

RELATED ARTICLES

LEAVE A REPLY

Please enter your comment!
Please enter your name here

- Advertisment -

Most Popular