Chipani cha UTM chati imfa ya Soldier Lucius Banda mnjowawa kwambiri maka pomwe chipanichi chikulirabe mtsogoleri wawo a Saulos Chilima.
Banda anali mkulu okopa (Campaign Director pachingerezi) anthu mchipani cha UTM.
Mneneri wa UTM a Felix Njawala wati ngati chipani sakudziwa kuti nkumatanino ndi momwe imfa yatengera akuluakulu ake motsogozana.
“Pomwe a Chilima ankachokera ku South Korea posachedwa, adadzera ku South Africa kukamuona Lucius Banda.
“Akuluakulu a chipani angapo akhalanso akukamuona. Sitinaganize kuti zithera chonchi. Kulira kwake ndiye nkumatani abale?” a Njawala awuza Times 360.