spot_img
Saturday, December 14, 2024
spot_img
HomeLatestKhoti lidzudzula apolisi pomanga anthu asanakonzeke ndi umboni

Khoti lidzudzula apolisi pomanga anthu asanakonzeke ndi umboni

Bwalo la milandu la Principal Resident Magistrate ku Lilongwe ladzudzula a police m’dziko muno ati kamba komanga anthu asanamalize kafukufuku wawo pa nkhani zomwe akuwaganizira.

Oweruza ku bwaloli, Rodrick Michongwe ndi yemwe wanena izi pomwe amapereka belo kwa m’busa wa mpingo wa CCAP mu synod ya Livingstonia, Kondwani Chimbirima atamangidwa pa mlandu ofalitsa uthenga osayenera pa masamba a mchezo.

A Michongwe akumbusa apolisiwa za kufunika komanga munthu atamaliza kafukufuku wawo ndipo awuzanso apolisa kuti adzitengera munthu amene amumanga kupolisi yomwe alinayo kufupi komanso ku bwalo la milandu lomwe wayandikana nalo osati kumupititsa polisi yakutali.

Malingana ndi oweruzayu, apolisi anamanga a Chimbirima asanamalize kafukufuku wawo, ndipo palibe umboni ogwirika pa nkhani yomwe akuwaganizira.

RELATED ARTICLES

LEAVE A REPLY

Please enter your comment!
Please enter your name here

- Advertisment -

Most Popular