Zaka 18 ku ndende kamba kodya “nyemba” ya nzake wapa mtima

0
368

Bwalo la Senior Resident Magistrate ku Limbe lagamula, Happy James, kuti akakhale ku ndende kwa zaka 18 kamba kogwirira mkazi wa bwenzi lake la pa mtima.

Bwaloli, lachiwiri, linamva kuchokera kwa oyimira boma pa milandu, Lloyd Magweje, kuti James anatengana ndi nzake wa pa mtimayu usiku wa pa 31 January chaka chino kupita kukaonera kanema ku Makheta m’tauni ya Machinjiri ku Blantyre.

Ali mkati mowonera kanemayu, James anamuzemba nzakeyu ndi kupita ku nyumba kwake komwe anakagwirira mkazi wa nzakeyu, pomwe anadzionetsera ngati ndi mamuna wake.

Koma akuti mkaziyo atazindikira kuti sanali mamuna wake, mpamene James anamuuza mkaziyo kuti anagwirizana ndi nzakeyo kuti asithane akazi kwa usiku umodzi, lomwe linali bodza.

Popereka chigamulo chake, Senior Resident Magistrate Ackia Mwanyongo, analamula James kuti akakhale kundende kwa zaka 18.

LEAVE A REPLY

Please enter your comment!
Please enter your name here