spot_img
spot_img
27.6 C
New York
Monday, August 8, 2022
spot_img
spot_img

Kodi nkulakwa kukhala mulhomwe? Mukutizunziranji?-Alomwe Afunsa A Chakwera

Kuchoka: Kwa Mafumu Onse a Mtundu wa Alhomwe, Utsogoleri wa Bungwe Lachikhalidwe la Mulhako wa Alhomwe, ndi Mtundu wa Alhomwe onse.

Kupita kwa: President wa Dziko la Malawi, Dr. Lazarus M. Chakwera, CC:

• District Commissioner

• Ministry of Homeland Security

• Ministry of National Unity and Civic Education

• Ministry of Culture and Tourism

• Public Affairs Committee and All Churches in Malawi

• Malawi Human Rights Commission (MHRC)

• Human Rights Defenders Coalition (HRDC)

• All Civil Society Organization in Malawi

• Country Ambassadors and Heads of Missions in Malawi

• All Media Houses in Malawi

Mutu:

Tikuyamba ndi funso lakuti, kodi nkulakwa kukhala mulhomwe? Kodi zomwe Alhomwe akuchitilidwa lero zikupeleka phunzilo lanji ku dziko la Malawi?

Ndizomvetsa chisoni, ndipo ndizoliritsa kuti mu nthawi tikukhalayi, munthu akhoza kuzunzidwa chifukwa cha mtundu wake. Timafuna tikumbutse mtundu wonse wa a Malawi kuti, sabata ziwiri zapitazi munthu wina otchedwa Silrage Phiri, kudzela mu audio message, ananyoza mtundu wa Chilhomwe. Zonsezi mkuluyu amayankha maganizo a munthu winaso otchedwa Ben Longwe, yemwe si munthu wa mtundu wa chilhomwe. Ben Longwe, amayankhula maganizo ake ngati mzika ya dziko lino kugwilitsa ntchito ufuru wake wamalankhulidwe pa kusowa kwa chilungamo ku Malawi kuno komaso zofooka ndi kulephela kwa utsogoleri mu nthambi zonse za boma ngati Nyumba ya Malamulo, Ma Court, nthambi za Chitetezo, zoona ndalama ngati Reserve Bank, MRA ndi ena. Chodabwitsa choyamba m’chakuti munthu wina anatengelapo

Kulira Kwa Alhomwe Pa Chizunzo Chomwe Akuchitilidwa

12th July, 2022

mwayi kuipitsa mbiri ya Alhomwe. Chodabwitsa chachiwiri ndichakuti, mabungwe omenyela ufulu wa anthu, Public Affairs Committee, Malawi Human Rights Commission, Human Rights Defender Coalition, Boma ndi ma unduna okhudzidwa ngati unduna oona za m’gwirizano komaso oona za chikhalidwe, onse angokhala chete. Chaka chathachi, nthawi ngati yomweyi, ife Alhomwe tinadandaula ku mtundu wa a Malawi za zomwe Alhomwe akukumana nazo. Mwa zina tinanenapo kuti lero Alhomwe akuzunzidwa kudzela mu njira izi:

1. Kuchotsedwa ntchito m’boma: poganizilidwa ndi kunamizilidwa milandu yomwe boma lilibe nayo umboni. Ena anachotsedwa ngakhale ma ofesi a kazembe a dziko lino.

2. Kuzunzika chifukwa cha ndale: Kusokoneza mtundu wa Chi Lhomwe ndi chipani cha DPP

3. Kusalidwa pa malonda: Alhomwe ambiri omwe ndiolimbikila pa okha, chifukwa choti ndi Alhomwe

akumanidwa ntchito za malonda za m’boma.

Mau athu ngati Alhomwe tikuti

• Choyamba: Ngati mtundu wa Alhomwe, kwathu ndiku Malawi kuno, makolo anthu ali konkuno,

tilibeso dziko lina. Kwathu ndikuno! Tinabadwila konkuno, tidzafela konkuno, palibe

otithamangitsa, ngakhale njira ya nkhondo.

• Chachiwiri: Alhomwe ndi mitundu yonse yakumwera, timakonda mtendere, timakonda kukhala

bwino ndi mitundu yina, m’chifukwa chake tikupezeka pena paliponse m’Malawi muno, ma state a fodya ku Kasungu Dowa ndi kwina, ma esiteti a sugar ku Nkhotakota, Chikwawa ndi kwina, tikupanga ma business madela onse. Amuna athu akwatila ku mitundu ina, ndipo akukhala nawo bwino, azimayi athu akwatiwa ndi azimuna a mitundu yina ndipo akukhala ma banja osangalara. Koma kukonda mtendere kwathu kusasokonezedwe ndikupusa. Ndife anthu, timamva uluru, ndipo ukaonjeza timatha kuchitapo kanthu.

• Kachitatu: Takhara mbali imodzi ya zochitika za dziko lino, kuthandizira ubwino wa dziko lino pa chitukuko ndi ndale, malonda, ulimi, kuyambila nthawi ya atsamunda, ulamuliro wa chipani chimodzi komaso wa zipani zambiri. Ife ndi mbali yayikulu ya dziko lino yomwe wina sangafufute.

• Kachinayi: Mtundu wa Alhomwe sichipani, ndipo sitidzakhala chipani. Chipani cha DPP chinapezeka patatha zaka zoposa 100 chibwelereni Alhomwe m’dziko muno. Kukhala muLhomwe umachita kubabwa, suchita kufunsila ngati umembala.

Chifukwa chani tikukamba izi? Kuyambira muchaka cha 2020 pomwe zipani zotsogozedwa ndi MCP zidapatsidwa mwayi oyendetsa dziko lino kwa zaka zina zisanu, zakhala zomvetsa chisoni kuti m’tundu wa Alhomwe kuphatikiza anthu onse omwe amachokela kuno ku m’mwera, akukumana ndi chinzuzo chachikulu. Kuyambila chaka 2020 Alhomwe omwe amagwila ntchito muma unduna, komaso nthambi ndi makampani a boma akhala akuchotsedwa ntchito pa zifukwa za ndale. Alhomwe ambiri kwa nthawi yayitali,

akhala akudzilimbikila pa okha, kuyambila nthawi ya chipani chimodzi pansi pa Dr. Kamuzu Banda, mu ndale za zipani zambiri pansi pa Dr. Bakili Muluzi, Dr. Bingu wa Mutharika, Dr. Joyce Banda, Professor Peter Muntharika kufikila lero. Ndi zomvetsa chisoni kuti anthu aluso komaso ophunzira bwino ngati awa akhoza kuzunzidwa, kulangidwa, chifukwa chakuti ndi Alhomwe. Ngakhale ana a chiLhomwe kuchita bwino ku sukulu ndi mulandu. Tikukumbuka ndichisoni ndikuwawidwa mtima pomwe Office ya Ombudsman mbuyomu inapeleka ganizo lofufuza ana athu aku Chambe ku Phalombe kuti afufuzidwe pa kakhozedwe kawo poganizilidwa kuti amachita za chinyengo, pamene ana amitundu ina akachita bwino dziko limayimbila m’manja. Lero aziphunzitsi athu olimbikila akusamutsidwa ndikuopsezedwa ndicholinga choti mtundu wa Alhomwe usachite bwino.

Ndizoona ndipo aliyense akhoza kuchitila umboni kuti kuyambila chaka cha 2020 boma lomwe likutsogozedwa ndi chipani cha MCP, chomwe mbiri ya Malawi imafotokoza bwino nkhanza zomwe limachitila anthu pansi pa m’tsogoleri wake woyamba malemu Dr. Kamuzu Banda likhozaso kutitengera kumbuyo. Munthawi yomwe iwo analibe owatsutsa, nthawi yomwe iyo analamula ndi nkhanza, kupha anthu osalakwa pazifukwa za ndale ndi nkhanza chabe. Nthawi yimeneyi, mtundu wa Alhomwe unanzuzikaso kwambiri. Tinaoneredwa pansi, ndipo nkhani za maphunziro, chuma ndi malonda sitinapatsidwe mwayi olingana ndi anzathu amitundu ina. Koma chifukwa cha khama lathu, kulimbika kwathu, tinapitiliza kuchita bwino, mu maphunziro ndi malonda. Nzosadabwitsa kuti lero Alhomwe ambiri kuchokela ku nyengo ngati izizi ndi ochita bwino. Lero, kuli Alhomwe ophunzira kwambiri dziko lino ndi kunja komwe, omwe sitiwatchula mayina awo lero. Kuli Alhomwe ochita bwino pa nkhani za malonda omwe sitiwatchula maina awo pano. Koma onsewa leroli, akutengedwa ngati achinyengo, mbava, zigawenga komaso osafunikila ku Malawi kuno.

Kuchokela mu chaka cha 2020, ife ngati m’tundu wa Alhomwe limodzi ndi abare athu akuno ku m’mwera, takhala tikuwona ndi kutsatira kayendetsedwe ka dziko lino, lomwe lagona pa tsankho komaso upo ofuna kuthana ndi mtundu wa Alhomwe. Izi zikunka zipitilila pomwe si anthu okhawo omwe ali m’maunduna, nthambi ndi makampani a boma omwe akuchotswedwa ntchito, komanso nkhondo yomwe inayambika yolimbana ndi Alhomwe omwe ndi ochita bwino. Taona ma kampani omwe anuwake ndi Alhomwe akukanizidwa kuchita malonda ndi boma. Komanso taona boma mwakhanza ndi upo ofuna kuthana ndi Alhomwe ochita bwino akufukula ndi kuyesetsa kulenga milandu pa zinthu zomwe ndizomvetsetseka malinga ndi m’gwirizano pakati pa opereka katundu (Kampani) ndi olipila (boma). Taona nthambi za boma zofufuza ndi za malumulo kuphatikiza a Police akuumirizidwa kulenga milandu yomwe ingapangitse mu Alhomwe aliyense ochita bwino kuti zinthu zimusokonokere.

Ndizomvetsa chisoni kuti lero, boma lasiya milandu yomwe iripo, yomwe yachitika posachedwapa, yomwe umboni wake ndioonekelatu nkumaononga ndalama pofuna kungoipitsa mbiri ya Alhomwe kuti adzioneka ngati anthu oyipa ndi osokoneza. Sizingakhale zolakwika kumuganizila m’kulu wachipongwe waku Lilongwe uja Sirage Phiri kuti amadziwa chomwe akunena ndipo anachita kutumidwa ndithu. Ndizomvetsa chisoni kuti m’malo moti boma liike chidwi chake pakuthetsa mabvuto omwe m’zika za dziko lino zikukumana nawo latanganidwa ndi zinthu zopanda pake. Zonsezi ndicholinga chongofuna kubisa kubvunda nd kulephela kwa utsogoleri wawo. Zinthu zikukwela mtengo tsiku ndi tsiku, anthu akulira tsiku ndi tsiku. Aliyense akungopanga zomwe akufuna pakuti palibe akuyang’anila zochitika za m’dziko muno. Boma likanaika nzeru ndi mphamvu kuthandiza a Malawi kuti mkati mwakubvuta kwa zinthu pa dziko lonse, uluru omwe nzikazi zikumva uchepeko. Koma lero liri patsogolo kuzunza ndi kulanga anthu osalakwa kalikonse.

Tikufuna titsindike pano kuti, zomwe Alhomwe ndi mitundu yonse yaku m’mwera kuno akuchitilidwa lero, zili ndikuthela kusokoneza Malawi yense. Chizunzo chomwe tikuchitilidwa, chili ndikuthekela koyambitsa kuukilana kwa m’tundu ndi m’tundu, ndikubala nkhondo ndikutayika kwa miyoyo yambiri. Taona izi zikuchitika ku Rwanda, Burundi, komanso mbiri ya dziko lonse ngati ku Germany. Izi sichilakolako cha muLhomwe aliyense wakufuna kwabwino. Choncho tikupempha dziko la Malawi, kudzela kwa President Chakwera, komanso nduna ndi nthambi zonse za boma, kuti pachitike zonse zothekela kuti m’chitidwe uwuwu omwe ungaike Malawi yense mu nkhondo yayikulu zipewedwe. M’chifukwa chake kudzela mu m’chikalata ichi tikukakamiza boma kuchita izi:

1. Boma lisiye kuzunza anthu akuno ku mwera, maka Alhomwe, podzela n’kuwaopseza ndi milandu yongolenga, kuchotsedwa ntchito kapena kukanizidwa mwai wa malonda ndi boma.

2. Mobwereza, uthenga kupita ku boma la Malawi, kudzela mu ma unduna okhudzidwa ayankhepo pa zomwe Bambo Silrage Phiri ananyoza mtundu onse wa Alhomwe.

3. Boma lithetse tsankho pa nkhani za malonda, maka maka ma contract a boma.

4. Pakhale chilungamo chosawona nkhope ya munthu, chipani ndi udindo pa ndale, mtundu kapena kapezedwe kamunthu pa nkhani za chilungamo ndipomwe munthu akuyenela kutetezedwa ndi

lamuloro.

5. Tikukakamiza boma kutsata chilungamo ndi kulemekeza lamulo ndi ufuru wa munthu pakafukufuku

ndi kufuna kudziwa nkhani zokhudzana ndi kampani ya Board Chairperson wa Mulhako wa Alhomwe, Mr. Leston Ted Mulli. Tikukakamiza boma kuti milandu yonse yongolengedwa yomwe ikungofuna kuwononga ndi kuthetsa kampani ya Mr. Mulli isiyidwiretu. Izi zikhaleso chimodzi ndi Alhomwe onse amene akudutsa mu nyengo ngati izizi kuphaitikizapo munthu aliyense wochita business m’Malawi muno.. Tonse tikudziwa mbiri ya Mr. Mulli, munthu yemwe ndiolimbika pa business. Iyoya anaphunzira business kuchoka kwa bambo awo, ndipo limodzi ndi azibale awo

agwira ntchito maluso ndi modzipereka ndipo lero kampani yawo ndi imodzi yayikuru m’Malawi muno yomwe mwiniwake ndi m’Malawi. Mr. Leston Mulli, wapereka ntchito kwa a Malawi oposa 3000, munthu yemwe alibe tsankho pakaperekedwe ka mwayi wa ntchito ku kampani yake. Kampani yake mukupezeka m’tundu wina uliwonse m’Malawi muno kuyambira kumpoto, pakati, ku m’mawa ndi ku mwera. Ndalama zake amapindula a Malawi a konkuno. Pakhale kutsata lamulo komaso umunthu pa nkhani zonse.

Tikulamula boma kuyankha madandaulo anthu wa pasanathe maola 24, ngati sitimva china chilichonse, ife ngati m’zika za dziko lino tili okonzeka kupanga zinthu izi malingana ndi zotiyenereze m’dziko muno:

1. MBINDIKILO m’maofesi onse boma, m’boma lirilonse mpaka zomwe tanenazi zitalemekezedwa. 2. KUCHITA ZIONETSELO ZA BATA NDI MTENDERE LACHINAYI LIRILONSE mpaka zomwe

tapempha m’kalata iyi zitalemekezedwa.

3. KUYAMBA KULIMBIKITSA LINGARILO LA ULAMULILO WACHITANGANYA (FEDERAL

GOVERNMENT), kuti aliyese akhale ndi ulamuliro onse pazochitika za m’chigawo chake.

Kwa Alhomwe komaso anthu mitundu yonse yokhudzidwa, tisalolere kuti kudzikonda kwa m’tundu umodzi, komaso kudzikweza kwa munthu m’modzi kuika dziko lino pa moto. Pali nthawi yoonerera zinthu, ndipo pali nthawi yopanga zinthu. Tidziwe kuti uwu ndi muvi, tikauonelera utilasa m’maso. Tonse tidzuke ndikuima pa ubwino waife, osalola wina kutitoza ndi kutionela pansi. Tili ndi dela, nzeru, mphamvu ndi zipangizo zotetezela ubwino wathu ngati m’zika za dziko lino. Izi ndizathu, ndipo nthawi yake ndi ino yoti tizigwilitse ntchito.

Pomaliza, kwa Alhomwe onse, mwa chikhalidwe chathu cha mtendere, mukupemphedwa kukhala olimbika kuposa kale. Mu umodzi muli mphamvu ndi chipambano. Mphamvu ndi umodzi wathu sizingadziwike ngati sitiyesedwa ndi nyengo ngati izi. Alhomwe amanyadila chikhalidwe chawo ndipo amakondwa ndi nsanamila za chikhalidwe chawo zomwe zimalunjika pa umodzi ndi kulorerana.

Mulungu Adalitse Malawi! Mulungu Adalitse Tonse!

Related Articles

LEAVE A REPLY

Please enter your comment!
Please enter your name here

- Advertisement -spot_img

Latest Articles

spot_img