spot_img
spot_img
17.1 C
New York
Saturday, May 21, 2022
spot_img
spot_img

Bwato Satsitsilana Pakati Pa Nyanja- Micheal Usi Wauza MCP

Nduna Yowona zokopa Alendo, a Micheal Usi, omwenso ndi wachiwiri kwa President wa chipani cha UTM, wauza President Lazarus Chakwera kuti chipani cha UTM chilibe lingaliro lotuluka mu Mgwirizano wa Tonse.

A Usi ayakhula izi Loweruka pa mwambo okumbukira mtsogoleri wakale wa dziko lino, a Dr. Hastings Kamuzu Banda, omwe ukuchitikira mu mzinda wa Lilongwe.

Mawu a Usi abwera pomwe akulu-akulu ena a chipani cha Malawi Congress (MCP) akufuna kuti chipani cha UTM chituluke mu Mgwirizano wa Tonse.

Usi ati kukakamiza UTM kutuluka mu Mgwirizano wa Tonse m’chimodzimodzi kukakamiza munthu kuti atsike mu bwato lili pakati pa Nyanja, zomwe malingana ndi a Usi ndi ichi ndi chipongwe komanso mwano.

Bwato satsitsilana pakati pa Nyanja,” anatero a Usi, powonjezera kunena kuti chipani cha UTM chipitiliza kulemekeza Mgwirizano wa Tonse.

Ndunayi yauzanso President Dr. Chakwera kuti achotse ntchito kagulu kena ka anthu komwe kakufuna kusokoneza Boma Lake.

Related Articles

LEAVE A REPLY

Please enter your comment!
Please enter your name here

spot_img
- Advertisement -

Latest Articles