Chilima Aletsa Chichewa Mu Khoti Kuti Anthu Asadziwe Choonadi

Oyendetsa mulandu womwe a Saulos Chilima ndi Lazarus Chakwera ananama kukhoti kuti aberedwa Chisankho anakonza kuti zokambirana zonse za m’Chizungu zitanthauziridwe m’Chichewa ndicholinga choti aMalawi tonse timve choonadi.

Koma mulandu wavuta kaamba koti aChilima akhalira kuchita chiphidigoliro ndimafunso chifukwa choti akulephera kuti anene bwino kuti anaberedwa motani.

A Chilima aliwuza khoti iwowo alibe vuto ndimavoti ndipo akudziwa kuti kuwelengera kunayenda bwino.

Atafunsidwa ngati chisankho chinaberedwa, kapena ngati a Professor Peter Mutharika anabela, a Chilima ananena kuti panalibe kubera.

A Chilima analiuza khoti sananene mchikalata chawo kuti wina anabera koma kungoti iwowo anadandaula kukhoti pazifukwa zina (osati kubera kapena kuti fraud) koma analephera kuliuza khoti zifukwa zinazo zosatchulikazo.

Apatu mpomwe mulandu unayamba kuchita chiphidigoliro a Chilima atayamba kugwa chagada ndi mafunso.

Maloya awo ataona aMalawi ayamba kuzimvera okha kuti aChilima anamiza aMalawi kuti chisankho chinaberedwa komanso kuti a Jane Ansah atule atule pansi udindo wawo anayamba kuvutitsa khoti mawayilesi onse asiye kuulutsa m’Chizungu.

Koma loya waboma a Kalekeni Kaphale analiuza khoti kuti likane kuletsa Chichewa chifukwa choti aMalawi onse ayenera azimvere okha kuti palibe vuto ndimavoti ndipo kuti a President Peter Mutharika anapambana bwino bwino.

Poweruza, khoti lalamula kuti mawayilesi apitirize kufalitsa zokambirana kukhotiko m’Chichewa kuti aliyense adziwe choonadi.

A Chilima akhala akuchita zionetsero, kuotcha maofesi ndi nyumba za anthu ponama kuti anaberedwa chisankho.

One Response to "Chilima Aletsa Chichewa Mu Khoti Kuti Anthu Asadziwe Choonadi"

  1. TMAN   August 11, 2019 at 8:17 pm

    Bwampini uyu,Chamba

    Reply

Leave a Reply

Your email address will not be published.